Friday, July 15, 2011

Zifukwa zomwe Amalawi apangire zionetsero pa 20 Julaye - Uthenga kuchokera kwa akonzi a zionetserozi


Mabungwe omwe akukonza zionetsero za Amalawi onse zosagwirizana ndi ulamuliro wa boma lilipoli apereka uthenga wa zina mwa zifukwa zomwe zawapangitsa kukonza zionetserozi. Ine monga m'malawi weniweni wolikonda dziko lake ndafuna tigawane uthengawu. Uthengawu, omwe uliponso chingerezi ndausindikiza m'musimu:


UTHENGA KWA A MALAWI ONSE PAMOMWE DZIKO LATHU LIKUYENDERA  NDIZOFUNIKA KUSINTHA.

Malawi Wabwino Ngotheka  !

Inu nonse a Malawi mukudziwa kuti mudzaka zisanu zoyamba za ulamuliro wa a pulezident Bingu wa Mutharika anthu tinatangwanika ndikuona ngati tiona zeni zeni ngati dziko. Ife ngati anthu amene timatsatira mwandondomeko zakayendetsedwe ka boma la democracy komanso potsatira zimene inu a Malawi eni munasankha mmene tinkasintha ulamuliro kuchoka ulamuliro wa chipani chimodzi mzaka za 1992 mpakana 1994.
Malawi tsopano wabwerera mbuyo ndipo wasanduka choseketsa cha anthu zifukwa za zinthu izi:-

  1. Kusowa ndalama za kunja zomwe timatha kugulira zinthu monga mankhwala, mafuta ndi zina zofunika.
  2. Kupereka bizinesi kwa anthu omwe ali pa ubale ndi pulezidenti ndi amtundu wake.
  3. Kusamvera malangizo ngakhale ochokera kwa atsogoleri a mipingo ndi zipembedzo.
  4. Kudzichemerera ndikusamvera kwake kwamtsogoleri wadziko lino
  5. Kufuna kusandutsa u pulezidenti ngati ufumu pofuna kusiira mng’ono wake mpando wa pulezidenti mopanda kutsatira ndondomeko zoyenera za demokalase ndi ulamuliro wabwino.
  6. Kuchitira nkhanza ndi kusawalemekeza a Malawi ena omwe agwira ntchito yokonza dziko la Malawi mbuyomu komanso ngakhale omwe iye wagwira nawo ntchito chifukwa chomulangiza.
  7. Kuthamangitsa anthu othandiza dziko lino komanso otigula malonda athu ngati fodya.
  8. Kuopyedza ufulu wachibadwidwe wa a Malawi poopsyedza atsogoleri a mabungwe omwe Sali a boma komanso manyuzipepala ndi mawailesi omwe Sali a boma.
  9. Posintha malamulo mosaganizira zomwe a Malawi anawaikira malamulowo ndizolingazo.
  10. Kusowa kwamafuta a magalimoto ndi zina zotero kwa nthawi yayitali.
  11. Kuletsa kugula mafuta mzigubu ngakhale galimoto itakuthera mafutawo panjira kapena kunyumba kwanu.
  12. Kunyozera zigamulo za ma khoti komanso kuopyeza ogwira ntchito mmakhotimo ndikuwamana malipilo awo motsutsana ndi malamulo.
  13. Kukondera popatsa maudindo a mboma ndi mabungwe aboma komanso business kwa anthu a mtundu wake wokha.
  14. Kuzunza atsogoleri akale ndi ena monga a pulezidenti opuma powakaniza kupita kuchipatala ndi achiwiri awe komanso a Chilumpha ndi a Vice Prezident a dziko lino  chifukwa choti ndi mzimai.
  15. Kuzikundikira chuma pogula ndi kumanga nyumba 15  kunja ndi kuno komwe pogwiritsa ndalama zomwe zikanatukula dziko lino.
  16. Kupatsa mkazache malipiro (salary) pogwira ntchito yothandiza yomwe ena amagwira osalipidwa.
  17. Kumangiridwa nyumba ndi zina ndi contractor yemwe akumpatsa ma contract a boma popanda ndondomeko.
  18. Kusamutsa university yoti imangidwe ku Lilongwe kuipititsa ku mudzi ndi munda wake ku Ndata ngati ndi yake
  19. Kumpatsa galimoto zomwe ziyenera kuyenda ndi anthu ngati pulezidenti ndi wachiwiri wake (convoy) kwa Peter Mutharika atalanda kw a Veep ndi a pulezidenti opuma pamene iye ali nduna wamba.
  20. Kulemba ntchito achibale ake mmaudindo akulu akulu a boma ndi mabungwe a boma.
  21. Kupereka chimanga mwaulere ku Zimbabwe mopanda chilolezo chochokera kunyumba ya malamulo.
  22. Kunamiza a Malawi kuti iye ngwa nzeru pamene akulephera kuyendetsa dziko.
  23. Kutseka sukulu zaukachenjede pamene analumbira kuti muulamuliro wake sukulu zimenezi sizizatsekedwanso.
  24. Kunyoza mavenda ndi anthu amalonda.
  25. Kuononga ndalama za boma pomanga damu kuNsanje popanda kuwafunsa a ku Mozambique omwe akukhudzidwa ndi mbali ina yantchitoyi.
  26. Kuwabera anthu omwe akupereka zinthu mboma ponama ndi nkhani ya funding.
  27. Kukhometsa misonkho mosaona kuvutika kwa anthu.
  28. Kuopsedza atsongolori a Zipani zotsutsa ndi amabubgwe amene si Aboma
  29. Kungwiritsa ndi kuphangira nyumba zaulusila mau za Amalawi (MBCTV) kutukwana amalawi.
  30. Kusapereka malipiro kwa Ziphunzitsi and ena ogwira Mmboma mu nthawi yoyenera 
  31. Kugwiritsa Ntchito Apolisi molakwika kutolera makobili Mmusewu ngati  MRA kutolera Misokho. 
  32. Kusakha popereka Chitukuko cha Dziko pokondera Madera ena monga kwawo kwa A Prezidenti

  33. Nkhani zonsezi ndi zina zotero zikuonetsa kuti akuluwa boma lawakanika kuliyendetsa- akuyesa kuti utsogoleri ndi njira yongolemelera ndikutchukapo. Tsopano nthawi yakwana kuti a Malawi tonse tidzuke ndikumuchotsa munthu wadyerayu pampando akupume kundende. Tikupempha a Malawionse kuti tigwirane manja kuti pa 20 July pano tichotse munthu ameneyu. Tipemphe achitetezo monga asilikali a nkhondo ndi apolisi kuti ateteze a  Malawi onse patsiku limeneli ndi masiku akubwerawa.

    Ife a Malawi okhudzidwa.

1 comment:

  1. We are a group of volunteers and starting a new scheme in our community.

    Your website provided us with valuable info to work on.

    You have done a formidable job and our entire community will be thankful to you.
    Feel free to surf my webpage : cheap strollers

    ReplyDelete

Comments